Mwamuna Aliyense Akwatire Akazi Asanu– Swaziland

Mfumu Swati yachitatu mdziko la Swaziland yapereka lamulo loti mwamuna aliyense akuyenera kukwatira akazi osachepera asanu mdzikolo apo biii apite ku ndende.

Malingana ndi uthenga omwe mfumuyi yatulutsa, boma lake ndi lomwe lidzalipira zonse pa nkhani ya mwambo wabanja komaso kugula nyumba zamabanjawo.

Mfumu Mswati yachenjeza kuti yense onyozera alandira chilango chokhwima.

Mfumuyi yati ikukhulupirira kuti izi zithandiza kuti akazi ambiri asakhale pamphala potengera kuti chiwerengero cha akazi nchochuluka poyerekezera ndi amuna

Kuonjezera apo boma la mfumu Mswati lapereka mwayi kwa amuna ochokera mmayiko ena maka a Kummwera kwa Africa kuti ngati angakonde apite mdzikolo kukakwatira akaziwa ndipo adzapatsidwa mwayi okhala nzika za dzikolo.

Mfumu Mswati mwiniyo ali ndi akazi khumi ndi asanu (15) pomwe bambo ake, omwe iyo idawalowa mmalo, adali ndi akazi 70.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *