Sindikupanga Nawo Za Ndale, Ndine Mtumiki Wa Mulungu–Bushiri

M’neneri Shepherd Bushiri wati alibe malingaliro ofuna kuyamba ndale kapena kupikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko chaka cha mawa.

A Bushiri, omwe ndi mtsogoleri wa mpingo wa ECG-The Jesus Nation ati iwo ndi mtumiki wa Mulungu amene cholinga chawo chakhazikika pogwira ntchito ndi boma lolamula ndipo adzapitiriza kutero.

Yemwe amawayankhulira, Aubrey Kusakala wati a Bushiri ndi wokhudzidwa ndi zimene anthu maka m’masamba a mchezo akhala akufalitsa kuti adzapikisana nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko.

A Kusakala apempha anthu amene akufalitsa izi kuti asiye kutero.
Pakadalipano, a Bushiri akuzungulira m’maboma a mdziko lino kugawa chimanga kwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala yomwe yayala mphasa.

Iwo adati akufuna kufikira anthu okwana 1 million ndi thandizoli.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *