Saturday, February 24
Shadow

Mafuta A Galimoto Avuta

Vuto lakusowa kwa mafuta a galimoto likupitilira kukhudza maboma ambiri ndipo boma la Ntcheu, oyendetsa galimoto kumeneku akukhala m’mizere kuti agule mafutawa.

Izi zakakamiza oyendetsa njinga zamoto kukweza mtengo onyamulira anthu akakwera njingazi kuzungulira pa boma ndi ndalama yokwana K500 yoonjezera, malinga ndi a Davie Maganga.

MFN Online itayendera malo anayi omwe amagulitsako mafuta a galimoto pa boma ku Ntcheu, malo a Petroda okha ndiomwe anali ndi mafuta a mtundu wa Diesel okha.

Masiku apitawa, wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la National Oil Company of Malawi-NOCMA a Hellen Buluma anauza Zodiak Online kuti dziko lino lili ndimafuta okwanira ndipo vutoli ladza kaamba kampani zogulitsa mafuta zina zikulephera kunyamula mafutawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *