Bwalo la magistrate ku Blantyre latulutsa pa belo yemwe anali wachiwiri kwa komishonala wa bungwe lotolela msonkho la MRA a Roza Mbilizi ndi anzawo ena awiri
Anthuwa anawamanga kaamba kowaganizira kuti adagwiritsa ntchito molakwika nambala yopelekera msonkho (TPIN) ya mtsogoleli wakale wa dziko lino a Peter Mutharika.
Bwaloli lalamula atatuwa kuti alipile K 350,000 ngati chikole komanso kuti apeleke ku bwaloli zikalata zawo zoyendera komanso anthuwa auzidwa kuti azikaonekera ku mafesi a ACB pa sabata ziwiri zili zonse
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!