CCTV Lati Zionetsero Zokhudza Ngozi Ya Ndege Ya Ku Chikangawa Zikhalepo
Bungwe la Concerned Citizens Timely Voice (CCTV) laikira kumbuyo ganizo la bungwe la CDEDI lochita ziwonetsero pa nkhani yokhudza ngozi ya ndege ya ku Chikangawa.
Malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa yati papita miyezi pafupifupi isanu ndi imodzi chichitikireni ngozi ya ndege-yi koma palibe cholozeka chomwe boma likunena zokhudza kukhazikitsa komiti ya padera kuti ifufuze za ngoziyi.
Read also: White House Security Incident: Secret Service Confirms No Threat to President Trump
Read also: Malawi belongs to its people, not individuals or parties—APM
Read also: BWATO SATSITSILANA PAKATI PA NYANJA”-Micheal Usi
Bungweli lapempha anthu onse omwe akufuna kudziwa chilungamo pa imfa ya Dr Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu kuti adzatenge nawo gawo pa ziwonetserozi.
Bungwe la CDEDI motsogozedwa ndi mkulu wa bungweli a Sylvester Namiwa akonza ziwonetsero lachinayi likubwerali pofuna kukakamiza mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti akhazikitse komiti ya padera kuti ifufuze bwino za ngoziyi ndikupeza mayankho a mafunso omwe aMalawi ali nawo okhudza ngoziyi.
Read also: Malawi at an Economic Crossroads: World Bank Warns of Costly Inaction
Read also: NAC Office Sealed
Read also: DPP leader Peter Mutharika whistle-stop tour in Blantyre





