DC wa boma la Lilongwe, Dr. Lawford Palani wauza gulu la Human Rights Ambassadors-HRA kuti lisachite zionetsero zake pa 28 September zofuna kuti President Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake, Dr. Saulos Chilima atule pansi maudindo awo ndipo kuti akalephera kutero aitanitse referendum.
Gululi likuganiza kuti a Chakwera ndi boma la Tonse alephera kuyendetsa dziko ati potengera mavuto omwe alipo pachuma, ufulu, ulamuliro wabwino komanso kusakwanilitsa malonjezo ambiri.
Koma Dr. Palani ati apolisi sadzatha kupereka chitetezo kamba koti adzakhala akupereka chitetezo m’malo omwetsera galimoto mafuta munzinda wa Lilongwe.
Mu kalata yawo yapa 22 September 2022, a Palani atinso apanga chiganizochi potengera zomwe akuti mkulu wagululi, Charles Ben Longwe wanena m’masamba a mchezo zomwe akuti zikulimbikitsa anthu kudzachita ziwawa patsikuli.
Koma m’modzi mwa omwe akonza zionetserozi, Redson Munlo wati iwo sakugwirizana ndi zifukwa zomwe akuluakulu munzindawu apereka ndipo wati apitiliza ndi ndondomeko yawo.
Munlo watinso pakadalipano apita kubwalo la milandu potsutsana ndi chiganizo cha adindo-chi.