Khoti Lati Zionetsero Za Mawa Zipitilire Ku Lilongwe

Bwalo la milandu lati ziwonetselo zomwe omenyela ofulu ena akonza mawa, Lachitatu munzinda wa Lilongwe zipitilire.

Oweruza milandu kubwalo lalikulu, Simeon Mdeza ndiye wapereka chigamulo-chi kuchotsa chiletso cha DC wa boma-li Dr. Lawford Palani.

Palani adaletsa zionetserozi ati poti apolisi atangwanika ndikupeleka chitetezo m’malo omwetsela mafuta a galimoto.

Komabe chigamulo-chi chati odandaula monga Kingsley Mpaso, bungwe la Human Rights Ambassadors, Ida Mazinga ndi Ben Longwe sakuyenela kutenga nawo mbali pa ziwonetselozi.

Izi zili chomwe-chi chifukwa choti pali mulandu wina omwe ena anakasumila anthuwa m’mwezi wa July chaka chino kuti asachititse ziwonetselo ati kaamba koti amalimbikitsa ziwawa.

Bwaloli lati m’modzi mwa odandaula yemwenso akukonza nawo zionetserozi, Redson Munlo atha kupitilira ndi zionetserozi koma awonetsetse kuti ndi za bata ndi mtendere.

Mwa zina, cholinga cha zionetserozi akuti nkufuna kuwuza President Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake, Dr. Saulos Chilima kuti atule pansi maudindo awo kapena kuti ayitanitse referendum ati kamba koti alephera kuyendetsa dziko lino.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *