Thabo Chakaka Nyirenda, yemwe amalangiza boma pa nkhani za malamulo, wati mlembi mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna zake, Colleen Zamba wachita bwino osakaonekera ku komiti ya Public Appointments-PAC ya nyumba ya malamulo pa nkhani yokhudza a Hellen Buluma.
Buluma, yemwe anali wachiwiri kwa mkulu wa bungwe NOCMA wauza PAC Lachitatu kuti a Zamba ankawakakamiza kupereka ma contract ogula mafuta mophwanya malamulo.
AZamba, omwenso ndi wapampando wa board ya NOCMA, sadapite kuti akafotokoze kumbali yawo pa nkhani-yi ngakhale adawaitana.
Koma a Chakaka Nyirenda auza wailesi ya Zodiak kuti PAC ilibe mphamvu yofufuza nkhani-yi koma komiti yowona za malamulo m’nyumbayi choncho aZamba achita bwino osamvera zomwe PAC inawawauza.
Koma komiti ya PAC yati ifunsa nzeru pa zomwe ikuyenera kuchita kutsatira kunyalanyaza kwa aZamba kosabwera atawaitana.
Wolemba: Martha Kachingwe Phiri-LILONGWE