Nkhalango Si Ya Joyce Kapena A Chakwera

FB IMG 1686621535969

Phungu wa Mwanza West, Joyce Chitsulo wauza anthu m’dera lake kuti adzisamala za chilengedwe maka nkhalango ya Thambani ponena kuti “nkhalangoyi si ya Joyce kapena a Chakwera koma ndi ya eni ake a derali.”

Iwo ati nzomvetsa chisoni kuona phiri la Thambani likutha chifukwa chakudula mitengo mwachisawawa.

FB IMG 1686621541702

Apa, phunguyu anauza anthuwa kuti alekeretu mchitidwe osakaza za chilengedwe ponena kuti adzavutika ndi mavuto a kusintha kwa nyengo komanso ena omwe amadza kamba kowononga nkhalango.

“Komano tithokoze kuti tinakhala pansi ndi mafumu, a Chigonjetso Community Based Organization ndipo tagwirizana njira zoti tichite kuti kuno kwathu kusapezeke galimoto lonyamula makala komanso munthu owotcha makala,” atero a Chitsulo

FB IMG 1686621553944

Phunguyu walankhula izi pomwe anali ndi mwambo okondwelera tsiku lake lakubadwa.

M’mawu ake, Senior Group Village Headman Tchale, omwe anayimira mfumu yaikulu Govati pamwambowu, yati agwiriza kugwira galimoto komanso kulanda makala kwa onse onyozera langizoli.

FB IMG 1686621547789

“Zikanakhala kuti makolo athu anali ndi mchitidwe wodzikondawu ife sitikadaiona nkhalangoyi. Tiyeni tonse tikondane posamala za chilengedwe komanso mitengo yathu m’derali,” yatero mfumuyi.

Nkhalango ya Thambani inali imodzi mwa nkhalango zomwe zidali ndi mitundu ya mitengo ya chilengedwe yambiri mdziko lino koma kaamba ka mchitidwe wosakaza mitundu idatha.

FB IMG 1686621560091

Anthu ambiri amaotcha makala pofuna kuphikira komanso kupeza ndalama.

Kafukufuku amasonyeza kuti anthu 15 okha mwa 100 alionse m’dziko muno ndi omwe ali ndi mwayi ogwiritsa ntchito magetsi koma boma lidati likulingalira kuti pofika 2030 aliyense adzakhale ali ndi magetsi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *