Dziko la United States of America lachenjedza dziko la Malawi kuti chuma chake chikugwa komaso silipasidwa thandizo lina lililonse kuchokela ku International Monetary Fund IMF ngati silisatila bwino mfundo zoliyeneleza kulandila gawo lachiwiri la Extended Credit Facility.
Dziko la USA layankhula izi pokwiya ndizomwe mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera akumachita posakaza chuma chadziko kuzela mu ntchito zakatangale ndimawulendo opanda phindu opita kunja kwadziko lino.
Poyankhula ndi antolankhani a MANA NEWS ONLINE munzinda wa Lilongwe, Eric Meyer yemwe ndi mlembi wachiwiri kunthambi yowona zachuma ku Africa ndiku Middle East wati dziko la Malawi likulephera kuwunikila bwino zakayendesedwe kachuma. Iye watinso boma likuyenela kuwonetsetsa kuti ndondomeko ya Integrated Financial Management and Information System (IFMIS) yakhazikitsidwa mwachangu.
Nthawi yomwe amakumana ndi nduna yazachuma ko