FB IMG 1724758340855

A Malawi adekhe: ntchito ili nkati–Kunkuyu

Chakwera adati lipoti latuluka kale–Chaponda

Boma lati lipoti lokhudza ngozi ya ndege yomwe inapha wachiwiri wakale kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Chilima komanso anthu ena asanu ndi atatu silinatuluke mpaka relo.

Malingana ndi kalata yomwe yasainidwa ndi mneneri wa boma a Moses Kunkuyu yati a katswiri a dziko la Germany omwe akufufuza za ngonizi anapeleka lipoti lapakamwa kwa akubanja pa zomwe anapeza pa malo omwe panachitikira ngozi yi.

Iwo akuti lipoti lenileni logwirika silinapelekedwe ku boma la Malawi.

Ndipo kaamba ka nkhani yomwe yi, kusamvana kunabuka ku nyumba ya malamulo pakati pa aphungu ambali yotsutsa ndi aphungu ambali ya boma mnyumba ya malamulo.

Kusamvanaku kunabwera pamene mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma ku nyumba yi, George Chaponda, anati akufuna kuti boma lipereke lipotili Ku mtundu wa a Malawi.

Izi zinadzetsa mkwiyo wa aphungu ambali ya boma pomwe anayamba kulankhula mau onyoza kwa mtsogoleri wa mbali yotsutsa bomayu.

Zinatengera mtsogoleri wa nyumbayi, Richard Chimwendo Banda, kufotokozera nyumbayi kuti zonse zokhudza lipotili zikatha boma lidzadzafotokozera mtundu wa a Malawi motsatira ndondomeko zoyenera.

Koma ngakhale izi zili chomwechi, mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera anati lipotili silinafikire ma ofesi ena oyenerera.

Chakwera amayankhapo pa funso lomwe anafunsidwa ndi mtolankhani wina wa wailesi ya DW.

Akatswiri ochokera m’dziko la German omwe akugwira ntchito yofufuzayi adati akwanitsa kupeza uthenga wotchedwa GPS momwe uli ndi kuthekera kofotokoza chomwe chinachititsa ngoziyi.

Kudzera pa tsamba la Internet la German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation (BFU), pakadali pano uthengawu uli m’manja mwa bungwelo ku German koma zitha kutenga nthawi kuti auunike bwino lomwe kuti choona chenicheni chidziwike.

Bungweli lidati pali kuthekera koti lipoti longoyembekezera litha kutuluka kumapeto kwa mwezi uno, ndipo lidzausindikiza pa tsamba lake la pa Internet la www.bfu-web.de/EN.

Bungweli lidatinso pambuyo pake kudzabwera lipoti lina lofotokoza mwa tchutchu chomwe chidachititsa ngoziyo, komanso kapewedwe kangozi zotero.

A Chilima, mayi wa fuko wakale wa dziko lino a Patricia Shanil Dzimbiri ndi anthu ena 7 anamwalira pa ngozi ya ndege pa 10 June chaka chino.

Iwo ankachokera mu mzinda wa Lilongwe kupita ku Mzuzu komwe ankayembekezera kukwera galimoto kupita m’boma la Nkhata Bay kukakhala nawo pa mwambo woika m’manda thupi la malemu Ralph Kasambara.

Boma lidapempha mamulumuzana ochokera ku German komwe ndegeyo, ya mtundu wa
Donnier 228-202(K), idapangidwa kuti lithandizire pa kafukufuku wa chomwe chidachititsa ngozi.

Akatswiriwa odachita kafukufukuyu m’dziko muno mu sabata imodzi ngoziyo itachitika.

More From Author

FB IMG 1724758340855 300x167

Investigation underway: Malawians could remain calm–Kunkuyu

FB IMG 1724769365977 300x135

UTM ikhala ndi msonkhano wosankha adindo pa 17 Nov

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Ella Brown

Project Manager

Darkness cannot drive out darkness; only light can do that. Hate cannot drive out hate: only love can do that.