UTM ikhala ndi msonkhano wosankha adindo pa 17 Nov

Chipani cha United Transformation Movement-UTM chatsimikiza kuti chichititsa msonkhano wake waukulu wosankha adindo achipanichi (Convention) pa 17 November chaka chino.

Mneneri wa chipanichi Felix Njawala ndiye wanena izi pa mkumano wa atolankhani omwe uli mkati pakadali pano mu mzinda wa Blantyre.

Njawala wati iwo akufuna kupititsa patsogolo khumbo la yemwe anali mtsogoleri wa chipanichi Dr. Saulos Chilima.

Iwo apempha, anthu omwe akufuna kudzapikisana nawo pa ma udindo osiyanasiyana kuti atsate ndondomeko zoyenera.

Mlembi wamkulu wa chipani Cha UTM Patricia Kaliati wati otsatira a chipanichi asamapitenso ku misonkhano ya boma komanso asamavale makaka achipanichi ku misonkhano yomwe siyachipanichi chifuwa sichilinso mu mgwirizano ndi chipani chilichonse pakadali pano.

Iwo ati chipanichi chati chizipita mu misonkhano yokhayo yomwe yakonzedwa ndi chipanichi osati yokonzedwa ndi boma.

Ndipo a Kaliati anenetsa kuti salola kutsatira mtsogoleri wa chipanichi Michael Usi ponena kuti iwo adatuluka mu mgwirizano wa Tonse.

Kaliati watinso amayi omwe adzapikisane nawo adzapereka theka la ndalama yolembetsera.

Naye mkulu wa achinyamata mchipanichi a Penjani Kaluwa wamema achinyamata kuti akapikisane nawo ku msonkhanowu chifuwa chipanichi chikulimbikitsanso utsogoleri wa achinyamata.

Kalua yemweso amadziwika bwino ndi dzina lokuti Fredokiss wapempha achinyamata m’dziko muno kuti alembetse mu kaundula wa unzika komanso umembala wa chipanichi.

Iye watinso achinyamata omwe aonetse chidwi chodzapikitsana m’mipando yosiyanasiyana adzapereka theka la ndalama zolembetsera.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *