Tikufuna kusula aphunzitsi kuti azipikisana ndi ena kunja kwa dziko lino – FAM

Football Association of Malawi (FAM) yati khumbo lawo ndilofuna kutulutsa chiwerengero chochuluka cha aphunzitsi a mpira wamiyendo oti azitha kumpikisana ndi aphunzitsi omwe akuchita bwino kunja kwa dziko lino.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa FAM, Christopher Madalitso Kuyera, walankhula izi lero, lachinayi, pa 29 August 2024 ku Mpira Village ku Chiwembe mu nzinda wa Blantyre pomwe amatsegulira maphunziro a aphunzitsi omwe akufuna kupeza tsamba la CAF B.

Kuyera watinso maso mphenya abungweli ndiofuna kukhala ndi aphunzitsi aukadaulo pofuna kukwaniritsa lingaliro lawo losintha masewerowa.

Mkulu wa bungwe la aphunzitsi, Aubrey Nankhuni, wathokoza utsogoleri wa Fleetwood Haiya omwe wapanga kuthekera kokhala ndi maphunzirowa.

Nankhuni wati anali ndi mavuto potulutsa maina a anthu omwe akuchita maphunziro wa potengera kuti chiwerengero cha aphunzitsi omwe alibe tsamba la CAF B ndi chokwera.

M’modzi mwa anthu omwe amalankhula mmalo mwa aphunzitsiwa, Victor Mphande, wayamikira FAM komanso bungweli kamba kochititsa maphunzirowa.

Captain John Kaputa komanso Technical Director wa FAM, Benjamin Kumwenda ndi ena mwa aphunzitsi omwe akuchititsa maphunzirowa omwe ndi amasiku 90 mmalo mwa bungwe la CAF.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Please disable your adblocker or whitelist this site!