Mpikisano wa Airtel Top 8

Tsiku lija ndi lero pamene mpikisano wa Airtel Top 8, za madolo, ukhale ukuyamba.

Akatswiri omwe akusunga ndi kuteteza chikhochi a FCB Nyasa Big Bullets ndi omwe atsekulire zonse pomwe akumane ndi timu ya Civo United pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Matimu awiriwa akukumana motsana mu chikho ndipo komaliza komwe adakumana padalinso pa bwalo lomweli pomwe FCB Nyasa Big Bullets idasosola nthenga Civo United 1-0.

Mawa lamulungu mu chikhochi ndiye kuli masewero awiri.

Mighty Mukuru Wanderers ikumana ndi Bangwe All Stars pa bwalo la Kamuzu pomwe ku Karonga kuli masewero a Chitipa United ndi Kamuzu Barracks.

Masewero ena adzakhalapo lachitatu likudzali pomwe Silver Strikers idzakumane ndi Premier Bet Dedza Dynamos pa bwalo la Silver mu mzinda wa Lilongwe.

Kumbukirani kuti mu ndime yoyambayi, matimu amabwerezana, pakhomo ndi koyenda.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Please disable your adblocker or whitelist this site!