MAYANKHO A HONOURABLE SAMEER SULEMAN PAKALATA YOMWE SIPIKALA WA NYUMBA YAMALAMULO ADAWALEMBERA PANKHANI YOKAYENDERA BUNGWE LA SFFRM POPANDA KUWADZIWITSA
Okupatsirani ndine
TWINK JONES GADAMA
- Ndinapita ku SFFRM ngati mzika yokhudziwa ndi kusapezeka kwa zipangizo zaulimi zotsika mtengo pamene nthawi yaulimi yafika. Ndinazindikira udindo wanga ofufuza chimene chikulepheretsa kupezeka kwa feteleza. Ngati mzika, ndili ndiufulu odziwa nkhani za feteleza amene ndiwanzika kuphatikizapo ine mwini. Pachifukwa ichi, ndinachiona chosafunika kudutsa njira zimene zinakhazikitsidwa kuti munthu ufikire ma bungwe aboma omwe ntchito zawo ndikuthandiza aMalawi kuphatikiza ine.
- Kuonjezera apo, anthu a m’dera limene ndimatumikira la Blantyre City South East ndiamene adandituma kuti ine ndipite ku SFFRM ndikafufuze chimene chikuchitika ndikuwabweretsera mayankho. Anthuwa ndiokhudzidwa ndipo ali ndinkhawa ndikuchedwa kwa ntchito yogulitsa zipangizo zaulimi zotsika mtengo chifukwa kufikira pano palibe wagulako m’dera langa. Ngati phungu wawo, ndinayenera kupita ku SFFRM mopanda kudziwitsa anthu kuti ndikazionere ndekha.
- Ndafunanso kuti ndikudziwitseni kuti ulendo wanga wadzidzidzi unatulutsa poyera zinthu zambiri. Mwachitsanzo, mkulu woyan’ganira malowa panthawiyi sanali pantchito. Ndinazungulira kuwasaka mpaka ndinafika kumene amasungira katundu. Ndie pokhala bungwe lofunika kwambiri, panthawiyi padalitu munthu m’modzi yekha mu ofesi. Ndikanatsatira ndondomeko zokhazikitsidwa kuti ndifike pamalowa, izi sindikanazipeza konse.
- Paulendo wanga ndidali ndi atolankhani kuti pakhale chilungamo. Sindinafune kuti ulendo wanga utanthauziridwe kapena kumveka molakwika. Ndinaonetsetsa kuti amalawi onse ndimbali imodzi yofuna kupeza zoona zake. Ulendo uwu sunali ofuna kuzikweza ndekha koma unali wa amalawi amene akudandaula kunjaku ndikusowa kwa zipangizo zaulimi.
- Monga ndikudziwira, palibe cholakwika atolankhani kupita Kumalo aboma kukajambula nkhani pokhapokha lamulo litawaletsa. Ndikukhulupila kuti SFFRM ilibe kuletsa kumeneko. Ulendo wangawu, olemekezeka a sipika, sunali wandale ai koma koma kukhudziwa ndi amalawi ochuluka amene akuvutika ndi kusayendetsa bwino nkhani ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo.
- Ulendo wangawu unathandiza ine pamodzi ndi dziko lonse kuzindikira kuti mavutowa sakubwera chifukwa cha SFFRM. Ndinazikira kuti kumene kumatulusa ndalama (treasury) ndikumene kwagona vuto. Izi ndinadziwa kudzera kwa mkulu wabungweri nditakumana nawo ku ULIMI HOUSE. Anandifotokozera ndondomeko yonse ndipo anandipempha kuti ndithandizire bungweri powuza a Treasury kuti atuluse ndalama kudzera kuma banki adziko muno popeza izi zatenga nthawi yaitali kwambiri.
- Potengera zomwe ndafotokozazi, ndine okondwa kukudziwitsani kuti ulendo umenewu udapindula. Nditangopita choncho, aku Treasury molumikizana ndima bank ena anatulusa ndalama kepereka kwa omwe anasankhidwa kuti atibweresere zipangizozi. Choncho m’malo modandaula ndinayembekeza mkulu wabungweri kuti andithokoza popangitsa ntchito yake kukhala yophweka.
- Ndili odabwa kwambiri ndizomwe mkulu wa SFFRM wachita podandaula ndiulendo wanga umene unali wabwino ndiothandiza amalawi. Pokhala mkulu wabungwe lofunika ngati ili, akuyenera kukhala omasuka ndiokonzeka kuchita mikumano ndizokambira ndi mzika. Mzika iliyonse ikhale ndimwayi ofika ndikupeza chilichonse chomwe angafune kwaiwo. Pasakhale kubisa pantchito zamabungwe aboma ngati SFFRM. Izi zimathandiza kuti pasakhale kugawana nkhani kapena mphekesera zabodza.
- Nkhaniyi ndiyofunika kwambiri, ndichiyembekezo changa kuti ofesi yanu pamodzi ndi aphungu ena onse tsiku lina mudzakhala nane m’maulendo otere. Monga phungu aliyense, ndikudziwa muli okhudzika ndikuchedwa kwa kwakupezeka kwa zipangizo zotsika mtengo monga m’mene timaganizira.
- Kutsatira ulendo wangawu, ndinapita kudera langa ndikukafotokoza izo ndinapeza. Anthu kwathu ndiokondwa kuti ulendowu unabala zipatso chifukwa ndondomeko zina zinayamba kuyenda . Komabe adakali ndinkhawa popeza kufikira pano sanagulebe feteleza.
- Potsiliza, ndikuthokozeni pondipatsa mwai kuti ndifotokoze mbali yanga. Ndi chikhulupiliro changa kuti kufotokozaku kumasula nkhawa zimene mkulu wa SFFRM anali nazo. Chomwechonso, ndikumpheni kuti mulangize mkulu wa SFFRM kuti nthawi ina akazakhala ndi nkhawa ngati izi, asazachedwe koma kundipeza ine mwini asadapititse nkhanizi ku ofesi yanu popeza ofesi yanu ndiyotangwanika nthawi zonse ndipo sikuyenera kumamva nkhani zopepuka ngati izi.
Ine,
Sameer Suleman, MP