Tikalembetse A Malawi Mkaundula wa Zisankho mphamvu ya kusintha dziko LINO ili mmanja mwathu

By Comrade jumbe

Pa chichewa pali mawu amatero kuti tsogolo ndi la iwo amene akukonzekera lero ,

Abale ndi alongo lero ndi mwayi wina wofunikira kwambiri kwa nzika iliyonse yomwe ikufunira zanwino dziko lino .

Mmene kalembera wa zisankho afika ku mapeto uwu ndi mwayi wathu womaliza wokonzekera kusintha komwe tonse amalawi takhala tikuyembekezera.

Chisankho chomwe chikubwerachi sichinthu chongochitika mwachizoloŵezi monga mwa nthawi zonse koma ndi nthawi yofunika kwambiri m’mbiri ya dziko lathu.

Kukhala chete osatenga nawo gawo liri lonse pa chisanko pamene ena akusankha tsogolo lathu ndi kuzimpwanyila tokha ufulu okonza tsogolo la dziko lathu chifukwa mphamvu zobweretsa kusintha zili mu voti yathu ndipo uwu ndi mwayi wotsiriza popeza kulembetsa kwa mec kwafika kumalecheleche.

Tiyenela kukumbukira kuti mtsinje umadzadza ndi dontho limozi limozi kulembetsa kwanu kungawoneke ngati kochepa koma kukalumikizana ndi mamiliyoni ena kumakhala mphamvu yomwe palibe munthu olo boma linganyalanyaze.

Ndikumema inu nonse amalawi kuti pitani mukalembetse mukawundula wazisankho auzeni anzanu akubanja lanu ndi aneba kuti achitenso chimodzimodzi.uwu ndi mwayi wathu kuti tichotse omwe alephera ndikusankha atsogoleri omwe adzayike miyoyo ya anthu patsogolo.

Chisankho cha mu September sichisankho chabe chifukwa amalawi talira kokwana ndipo tikulira kotero ndi nthawi yathu yobweretsa kusintha komwe takhala tikudikirira.

Kalembetseni lero ndikuteteza liwu lanu pokonza tsogolo la dziko lathu. mphamvu ili m’manja mwathu tiyeni tigwiritseni ntchito mwanzeru .

pamodzi tingathe

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *