Mkazi Wabwino

BANJA

  1. Mkazi akakhala wodzichepetsa amakhala ngati chithumwa chachilengedwe kwa mwamuna wake.
  2. Mkazi akakhala wogonjera, amapeza zimene akufuna kwa mwamuna wake
  3. Mkazi akakhala wodalirika, amatha kulamulira chuma cha mwamuna wake
  4. Mkazi akakhala wochezeka, akhoza kuchepetsa maendedwe a mwamuna wake
  5. Mkazi akakhala ofikirika, amakhala bwenzi lapamtima la mwamuna wake
  6. Mkazi akakhala wanthabwala komanso wokonda kuseŵera, amatha kuchitsa nkhawa za mwamuna wake
  7. Mkazi akakhala woyamikira, amalandira mphatso zosayembekezereka kuchokera kwa mwamuna wake
  8. Mkazi akakhala waulemu, angapite naye kumisonkhano ya chikhalidwe cha mwamuna wake
  9. Mkazi akakhala omvera, mwamuna wake amamasuka kumuuza ngakhale zoipa
  10. Mkazi akakhala wamtendere, mwamuna wake amabwera mothamangira kunyumba nthawi iliyonse
  11. Mkazi akakhala ndi mtima wofewa, amakhala mayi olera beino ana ake
  12. Mkazi akakhala wodekha, amadziwa nthawi yoti alankhule ndi mwamuna wake pa nthawi ya kusamvana ndi kukangana.
  13. Mkazi akakhala kuti alibe vuto, amakondedwa ndi mwamuna wake
  14. Mkazi akakhala kuti samubisira mwamuna wake, mwamuna wake amamuuza zonse zomwe akuchita
  15. Mayi akamapemphera, amakhala wothandiza kwambiri kwa mwamuna wake
  16. Mkazi akakhala woopa Mulungu, nyumba yake imakhazikika pamalamulo a Mulungu Wamphamvuyonse.
  17. Mkazi akakhala wopanda dyera, mwamuna wake amadalira iye kotheratu
  18. Mkazi akakhala othamanga thamanga,(creative woman), iye ndi mwamuna wake amatha kudziwa tsogolo limodzi

Tsoka ngati simuli mmodzi wa awa, zimakhala zovuta kuti musangalale m’banja.

Pemphani Mulungu kuti akuthandizeni kukhala mu mzonse mwa izi ndalemba pamwambazi, simungathe kuchita nokha.

Moni kwa Akazi nonse omvera muno

MKAZI WABWINO AMANGA BANJA LAKE YEKHA (Miyambo 31:10-31)

Zonse zimayamba ndife za muno muchipatala.

Moyo ndi mpamba usamalireni lero.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *