
Uku kunali kung’ung’uza kwa anthu ena omwe amachokera ku bwalo la masewero la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre komwe kunali masewero a pakati pa timu Ekhaya ndi timu ya Tigers amu mpikisano wa Tnm Super League.
Ekhaya FC yomwe yalowa mu mpikisano wa Tnm Super League koyamba, yapambana masewero ake oyambanso pogonjetsa Tigers 2 kwa duu kupyolera mu zigoli za Lovemore Mbeta ndi Emmanuel Savieli.
Kupambana kwa Ekhaya kwatengera timuyi pa mwamba pa Ligi kamba ka zigoli poti ngakhale ma timu Bullets ndi Mafco nawo apambana masewero awo, ndi Ekhaya yokha yomwe yamwetsa zigoli ziwiri.
M’modzi mwa akuluakulu a masapota a Ekhaya FC anauza Times 360 Malawi kuti iwo abwera kudzakhala ndipo ma timu achenjele chifukwa wina alira.
Mayekha popita mutitengeee!
Mayekha popita mutitengeee!
Lero limenelo lero, Lero limenero lero!….!
Kunali kuyimba uku galimoto zikungoliza mahutala ndipo ena akung’ung’uza.
Zotsatila za masewero onse omwe aseweledwa lero
Silver Strikers 0 – FCB Nyasa Big Bullets 1
Mafco 1 – Chitipa United 0
Ekhaya FC 2 – Mighty Tigers 0