President wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wayamika kampani zonse zomwe zidamvana ndikuyika ndalama zawo pamodzi kuti amange Protea Hotel Lilongwe Ryalls.
Mtsogoleri wadziko linoyu wati zimenezi zaonetsa mtima odzidalira pakati pa kampani zachi Malawi.
Dr Chakwera walankhula zimenezi ku Lilongwe atayendera ntchito yomanga hotelayi, yomwe akuyimanga ku Lilongwe Golf Club.
“Ine ndakhutira kwambiri ndi zomwe ndaona, ngati hotelayi ikuoneka bwino chonchi, koma siyinathe, kuli bwanji ikatha…”
Pa nkhani ya ndalama zakunja, zomwe akugwiritsa ntchito poyitanitsa katundu pamalopa, Dr Chakwera watsimikizira a Nico, Blantyre Hotels ndi onse.kuti boma lionetsetsa.kuti ndalama zakunja (Forex) zikupezeka mpaka ntchitoyi idzathe.
M’mau ake, Wapampando wa Blantyre Hotels, Vizenge Kumwenda, wayamika boma boma popereka mpata kuti kampani zachiMalawi zithandizepo pa ntchito zokopa alendo.
Komabe iwo apemphanso boma, kudzera ku unduna waza maboma ang’ono, kuti usamutse malo okwelera minibus apa labour chifukwa ali pafupi ndi hotelayi.
Protea Hotel Lilongwe Ryalls idzakhala ndima lumu 180, komanso malo ochitiramo misonkhano, mwa zina chabe.