Muluzi wadandaula ndi umphawi wa A Malawi

Mtsogoleri wa chipani cha UDF Atupele Muluzi, wakhazikitsa ndondomeko ya tsopano ya momwe a Malawi angatukukile, yomwe pachingelezi ndi Business First.

A Muluzi atsindindika za momwe a Malawi akuyenela kuganizila za tsogolo lawo pa nkhani ya kayendetsedwe ka dziko lino.

Iwo anati chiwelengelo cha anthu osauka chakwela kwambili kuchokela mu chaka cha 2020 zomwe zikuyika miyoyo ya anthu kupitilila kusauka ngat satengapo gawo posintha utsogoleri omwe ulipowu.

Malawi ngati dziko imapanga ndalama pafupifupi 1 billion ya ku America pa chaka yomwe ndi ndalama yochepa kutengela ndi ndalama yomwe imafunikila kuti dziko lino lilowetse katundu ofunikila m’dziko muno yomwe ndalama yake ndiokwana 3.2 billion ya dziko la America.

Mu ndondomekoyi anthu osaukitsitsa adzakhala ndi chakudya chokwanila kutengela kuti adzabweletsa ndondomeko zoyenela za momwe alimi angapezeke feteleza komanso chakudya chotchipa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *