By Mabvuto Kalawa
Pali mwambi wakale woti “chinenepetsa nkhumba sichiziwika,” zomwe zikugwirizana bwino ndi ntchito yolimbika yomwe ikuchitidwa ndi Bambo Mustard Gobede, yemwe ali ndi zaka 45 zakubadwa.
Bambo Gobede amachokera m’mudzi mwa Nyakwawa Mchakulu, ku chigawo cha mfumu yaikulu Ndodo, m’boma la Lilongwe.
Ali pa banja ndipo ali ndi ana awiri.
Pakulankhula ndi mtolankhani, Bambo Gobede anafotokoza kuti anayamba ntchito ya ulimi chifukwa cha kusowa kwa ntchito.
Iwo anati sanali ofuna kuti pakhomo pawo pakhale kusowa kwa chakudya kapena ndalama, choncho anaganiza zoyamba kulima.
Kupatula ulimi odalira mvula, monga kulima chimanga, mbatata, ndi chinangwa, Bambo Gobede ali ndi dimba lamadzi lomwe amalima tomato, sabola, komanso zipatso monga mango, nthochi, mapapaya ndi nzimbe.
Iye ananenanso kuti amagwiritsa ntchito njira zonse za ulimi wamvula ndi ulimi othirira.
Kuphatikiza ndi mbewu, Bambo Gobede amalimanso nthochi zambiri.
Ali ndi nkhumba zomwe amaweta pakhomo pake.
Komanso, ali ndi maiwe atatu omwe akuwetamo nsomba zosiyanasiyana monga chambo, milamba, ndi zina.
Pofunsidwa za phindu limene akulandira mu ulimi wake, Bambo Gobede anati ntchito ya ulimi yamsandutsa moyo.
Iye anati wapindula kwambiri moti anagula ma pump awiri; imodzi imagwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa ndipo inayo imagwiritsa ntchito mafuta.
Alinso ndi njinga yamoto yomwe amagwiritsa ntchito paulimi ndi mayendedwe.
Anamanganso nyumba ya malata komanso ali ndi grocery yomwe imathandiza pakhomo.
M’banja mwake muli pamwana alirenji ndipo chakudya chili chokwanira nthawi zonse.
Ananenanso kuti chimanga chimene amalima amachigulitsa ndipo ana ake akupita kusukulu bwino.
Pamavuto omwe amakumana nawo paulimi, Bambo Gobede anatchula kukwera kwa mitengo ya zipangizo za ulimi monga feteleza.
Ngakhale ali mu kalabu ya alimi a nsomba, Bambo Gobede anati akukumana ndi vuto la kusowa kwa misika.
Ananenanso kuti alangizi a zaulimi sakuwafikira kuti awalangize bwino.
Ananenanso za chaka chimene nthochi zao zinagwidwa ndi matenda, ndipo atafunsa anzake, anauzidwa kuti otche ndi kulima zina.
Chaka chino, amavutikanso chifukwa chimodzi mwa maiwe awo chaphwera ndipo nsomba zikufa.
Komanso akuba amafika ndi kuba zinthu zomwe wakonza ndi kulima mwakhama.
Pofotokoza zomwe akufuna kuchita mtsogolo, Bambo Gobede anati akufuna kupeza misika yokhazikika komanso yodalirika.
Iye akufunanso kugula galimoto kuti azinyamulira katundu wake, chifukwa panopa amagwiritsa ntchito ngolo yokha.
Pempho lake kwa boma ndi mabungwe ndikuti amuthandize ndi zipangizo za makono komanso athandizidwe kupeza misika yokhazikika ya malonda ake.
Langizo lake kwa alimi anzake ndi lakuti azitenga ulimi ngati bizinesi.
Anati alimi asamaziyang’anire pansi ntchito ya ulimi, ngakhale alangizi sawayendera.
Iye anapitiriza kunena kuti alimi ayenera kufunsana ndi anzawo omwe akuchita bwino mu ulimi ngati njira yophunzira ndiponso kupita patsogolo.
Bambo Mustard Gobede akuyimira chitsanzo cha mmene kudzipereka, kulimbikira, komanso kukhala ndi masomphenya kungasinthe miyoyo ya anthu kudzera mu ulimi wamakono.