Mangochi, Malawi – June 16, 2025
Kuvuta kwa mafuta a galimoto kwafika pa mpondachimera m’boma la Mangochi, komwe lita imodzi ya mafuta tsopano ikugulitsidwa pa mtengo wa K15,000 kudzera kwa mavenda osavomerezeka. Zomwe zachititsa chipwirikiti pa mtengo wa maulendo ndiponso kuyamba kwa befu looneka.
Malingana ndi kafukufuku wathu, mitengo ya ulendo yapita patali kwambiri kuposa momwe zinali kale. Pa Lolemba ino, tsiku la 16 June, anthu akuyenera kulipira pakati pa K35,000 ndi K40,000 kuti afike ku Blantyre — mtunda womwe nthawi zambiri umalipidwa K15,000 yokha.
“Masiku apitawa ku Blantyre timakwera pa K15,000 koma pano akutikakamiza kuti tikwere pa mtengo wa K40,000 kapena K35,000. Zomwe ambiri mwa ife sitingakwanitse,” watero mmodzi mwa apaulendo amene tacheza naye ku Mangochi.
Mavuto a mafuta awononga kwambiri malonda, monga momwe a Adam Matola, omwe amagulitsa mafuta, adalankhulira.
“Takhala pano kuyambira dzulo koma palibe chiyembekezo. Kodi uwu ndi moyo wanji, kodi tikhalira izi mpaka liti?” adafunsa Matola mokhumudwa, poyang’ana pa ng’oma zopanda mafuta zomwe nthawi zonse zinkakhala zodzaza.
Nkhaniyi ikuchitika pamene Purezidenti wa Dziko lino, a Lazarus Chakwera, ali m’dziko lomaliza ntchito zina za boma, osatchula momwe akonzekera kuthana ndi kusowa kwa mafuta kumeneku komwe kwasokoneza miyoyo ya anthu ambiri.
Pofika pano, anthu ambiri akuyembekezera mawu kuchokera kuboma lomwe silinapereke yankho lomveka, pomwe mavenda akupitiriza kutenga mwayi wavutoli podula mitengo.
Maulendo, bizinesi, komanso moyo watsiku ndi tsiku wakumana ndi chiyeso chachikulu — ndipo anthu akudzifunsa: Kodi vutoli litathe liti?