President Lazarus Chakwera dzulo lachitatu anapanga mkumano wapadera ndi President wa dziko la Zambia Hakainde Hichilema pambali pa mkumano wa atsogoleri amu bungwe la SADC omwe uli mkati m’dziko la Democratic Republic of Congo.
Polemba pa tsamba lawo la Facebook, Dr Chakwera anati iwo ndi a Hichilema anakambilana nkhani zingapo kuphatikizapo ndondomeko yolimbikitsa ntchito za malonda pakati pa maiko awiliwa.
Kumbali yake, Dr Chakwera anayamikira a Hichilema komanso dziko la Zambia pazomwe lidachita ponjata mzika ya dziko la China yotchedwa Lu Ke (Susu) yomwe pakadali pano ili kuno kumudzi kuyankha milandu yopanga za kusayeluzika pogwilitsa ntchito ana akwa Njewa Ku Lilongwe.
Iwo anayamikilanso boma la Zambia kaamba kothandizapo pa ndondomeko yotumiza kuno kumudzi matupi a ogwira ntchito atatu a bungwe la Central Medical stores trust omwe adafa pangozi ya galimoto ku Zambia.