Minister of Information Gospel Kazako yawopseza makampani opanga mafuta ophikira kuti boma likhoza kuyambitsa kampani yake yopanga mafuta ngati mitengo sitsika.
A Kazako anena izi pokambirana ndi atolankhani a boma mu mzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi a Kazako n’zachisoni kuti mitengo ya mafuta ophikira ikukwerabe ngakhale boma likuchitapo kanthu pa madandaulo awo a msonkho.
Mwezi watha, Nduna ya Zachuma Sosten Gwengwe adalengeza za kuchotsa msonkho wa Value Added Tax (VAT) pamafuta ophikira ndi zinthu zina.
Amalawi ankayembekezera kuti mitengo ya mafuta idzatsika mwatsoka, mitengo ikukwerabe.“`