“Tikuzunzika Tipatseni Malipiro Athu

Anthu ena ogwira ntchito ku bungwe la ADMARC adandaula kuti akuzunzika komanso kuponderezedwa kuchokera pomwe boma lidatseka bungweli kuti likonze zinthu.

Izi azinena pomwe anthu oposa 300 ogwira ntchito ku bungweli achita zionetsero m’mawawu pofuna kukamiza boma kuti liwapatse malipiro awo a mwezi wa September ndi October.

Iwo akufunanso boma lichite machawi pokonzanso zinthu ku bungweli.

Ambiri mwa omwe amachita zionetserozi anavala makaka akuda.

Anthu okwana 4687 akuyembekezeka kuchotsedwa ntchito ku ADMARC pomwe boma likuti likufuna kukonzanso ntchito za bungweli pomwe zikumveka kuti ogwira ntchito ena amasaka chuma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *