Mkulu wa kampani ya Kachere Agriculture Trading, Smolet Kachere wati pali mbava zambiri zikuluzikuli zomwe zikukhudzidwa ndi kusowa kwa chimanga ku bungwe la ADMARC zomwe zikuyesetsa kusokoneza contract yawo.
Iye wanena izi pomwe komiti ya nyumba ya malamulo yamubweza kaye pa kafukufuku okhudza kusowa kwa chimanga ku ADMARC ati kamba koti nkhani-yi ili ku khothi.
“Akuti ali ndi chimanga chokwana ma tani 38,000 koma kukuuzani zoona chimanga chomwe chili ku ma depoti a ADMARC mchochepa chifukwa anthu achiba,” watero Kachere
Iye watsimikiza kuti omwe akuba chimangachi ndi mbava zikuluzikulu ndipo kafalitsidwe ka nkhaniyi kakulandira thandizo lambiri kuti umbavawu usadziwike ndi aMalawi.
Kachere amawonekera ku komitiyi lero kuti afotokoze mbali yake pomwe kampani yake akuiganizira kuti idasowetsa chimanga cha ndalama zokwana 112 million kwacha.