“Mlembi wamkulu mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino Colleen Zamba, amakakamiza bungwe la NOCMA kuti lichite chinyengo pogula mafuta.”
Izi zaululika lero pomwe yemwe anali ogwirizira udindo wa mkulu wa bungwe la NOCMA, Hellen Buluma, anakaonekera ku komiti ya nyumba yamalamulo yowona zakalembedwe ka ntchito ka anthu m’boma.
Buluma anati amakakamizidwa ndi Zamba kuti apereke mwai obweretsa mafuta mdziko muno kwa munthu wina wa dziko la Nigeria yemwe amangodziwika kuti Chief komanso munthu wina yemwe akuti ndi Evarista Kamwangala, yemwe akukhala ku South Africa.
Ngati wapampando wa bungwe la NOCMA, Zamba amayenera kuonekera ku komitiyi masanawa pamodzi ndi amnzake koma sanafike ndipo sanapereke chifukwa chilichonse.