Zambiri zayankhulidwa ndipo anthu ochuluka apereka maganizo awo pa zomwe akuganiza kuti ndi zifukwa zomwe Hon. Mchacha achotsedwera pa udindo wawo muchipani cha DPP. Ngakhale zambiri zayankhulidwa, chowona chake pa nkhaniyi ndi chakuti olemekezeka bambo Mchacha achotsedwa pa udindo wawo chifukwa chosowa khalidwe. Ndipo izi zawonekera poyera posachedwapa pamene Olemekezeka Bambo Mchacha anayankhula mau onyoza pagulu kunyoza Vice President wa chipani cha DPP kuchigawo chakumwera pa nthawi imene APM amakayendera anthu amene anakhudzidwa ndi namondwe wa Freddy ku Luchenza.
Kunyoza kumene olemekezeka a Mchacha ananyoza mtsogoleri mzawo wa muchipani ndi zotsutsana kwambiri ndi chitsogozo chomwe Mtsogoleri wa chipani cha DPP, Prof. Mutharika anapereka komanso kuyankhula poyera ku msonkhano wa ku Mangochi. Prof. Mutharika anawuza adindo onse a mu chipani kuti mpofunika kulemekezana ngati njira imodzi yolimbikitsira umodzi mu chipani cha DPP.
A President Mutharika atawadzudzula a Mchacha za khalidwe lawo lonyoza anzawo a mu chipani, a Mchacha nkhani iyi sanailandire bwino ndipo mmalo mwake anamemeza ma District gavana a muchigawo chakumwera nkuwaitanira ku office ya region komwe a Mchacha anayankhula mau onyoza kunyoza Prezidenti Mutharika. Mmau awo, a Mchacha anauza ma gavanala omwe anasonkhana kuti nzoduka mutu kulora a Mutharika kuti aimenso pa mpando chifukwa akhonza kudzafera mu office. Izi sizidakondweretse magavanalawa potengera kuti mmomwe anankhulira a Mchacha nzosemphana kwambiri ndi chikhalidwe chathu ngati a Malawi.
Kupatula nkhani yonyoza atsogoleri anzawo, Olemekeza a Mchacha ali ndi mbiri yonyoza atolankhani zimene ndi zotsutsana ndi Mfundo zoyendetsera chipani cha DPP. Pakadali pano, pamene chipani chikuzikonzanso, mpofunika kuti adindo muchipanichi asakhale a ma phunzo koma olemekeza Mfundo zonse za mu ulamuliro wa demokalase.
China chimene utsogoleri wa chipanichi waganizira kuti mpoyenera kuti a Mchacha achotsedwe ndi chakuti; Pamene kuli ma candidate osiyanasiyana amene akufuna kudzapikisana nawo ku msonkhano waukulu wa chipanichi, zimaoneka kuti a Mchacha amabereka candidate wina ndipo ma candidate ena samawapatsa mwai ofanana ku chigawo chimene iwo amayang’anira.
A Mchacha akhala pa udindo wa u Regional Gavanala pafupifupi zaka zokwana zisani ndi zitatu (8) ndipo mu nthawi yawo agwira ntchito zosiyanasiyana zotumikira chipani cha DPP. Chofunika ndi chakuti Olemekezeka a Mchacha alingalire bwinobwino ndi kukonzanso khalidwe lawo kuti tsogolo lawo pa ndale likhale lowala!