
Tony Ngalande
Phungu wa dera la kumpoto kwa boma la Balaka a Tony Ngalande wakhazikitsa ntchito yokonza misewu imene idaonongeka kumayambiliro a chaka chino kaamba ka namondwe wa Freddy, ngati njira imodzi yofuna kuonetsetsa kuti ntchito za malonda zikupitilira m’derali.
Poyankhula pamene amakhazikitsa ntchitoyi, a Ngalande adati iwo achita izi pofuna kuonetsetsa kuti anthu a madera osiyanasiyana kuzungulira bomali akhale ndi mayendedwe abwino, pofuna kupititsa patsogolo ntchito za malonda.
Pa mwambowu, phunguyu anaperekanso zofunda kwa anthu achikulire ndi ovutika okwana 200 komanso cheke cha ndalama zokwana K8 miliyoni ngati ngongole ku magulu a amayi komanso achinyamata.
Mayi Magret Msanama a zaka 76, a dera la Kandengwe ayamikira phunguyu kaamba ka thandizoli ponena kuti liwanthandiza kwambiri mu nyengo ino yozizira.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!