Nkhope za ochemelera a FCB Nyasa Big Bullets zikupitilirabe kulemedwa ndichisangalaro pamene timuyi yagonjetsa Moyale Barracks 3-1 mumasemifainolo a FDH Bank Cup pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.
Chipambanochi chikudza, patangodutsa masiku atatu timu yovala zoyera ndi zofiirayi itagonjetsa Red Arrows ya m’dziko la Zambia 2-1 mumasewero oyamba a CAF Champions League.
Chigoli chimodzi kuchokera kwa Ephraim Kondowe komanso zigoli ziwiri kuchokera kwa Babatunde Adepoju, pamene Emmanuel Allan, ndi yemwe anagoletsa chigoli chopukutira misozi kwa asilikaliwa.
Potsatira chipambanochi, Mapale adzakumana ndi Blue Eagles FC mu ndime yotsiliza yampikisanowu.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!