Mphunzitsi wa timu ya Malawi Patrick Mabedi wati ngati mphunzitsi pena zimayenera kuoneka ngati wamwano kuti zinthu zina ziyende.
Iye amayankhula izi poyankha mafunso kwa atolankhani pakutha pa masewero omwe timu ya Malawi yagonja 3-2 ndi Burundi.
Iye wati anthu ochemelera amaonera mpira mosiyana ndi momwe iwo ngati ophunzitsa amaonera.
Mabedi amayankha funso pa chifukwa chomwe amamutulutsira Yamikani Chester pomwe ochemelera amaona kuti akuthandiza timuyi.
Koma poyankhapo ngati alibe nkhawa ndi mkuwe omwe ochemelera amachita timuyi itagonja, iye adati sakutekeseka, akuti iwo akuwidwako ngati osewera ndipo mkuwe wa dzulo mwinaso unachepa.
Malawi ikuyembekezeka kusewera ndi Burkina Faso lachiwiri likubwerali m’dziko la Mali pa masewero ake a chiwiri mu ndime yodzigulira malo ku mpikisano wa 2025 Afcon.
Wolemba: Promise Thom
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!
