Phungu wa dera la Machinga East a Esther Jolobala wati mngodabwa kuti nthambi ya NRB siidayambebe kulemekeza chigamulo cha khothi chomwe chinapelekedwa Lachisanu lapitalo.
Mwa zina, khothi lidalamula NRB kumalembetsa anthu ziphaso zaunzika mmalo momwe bungwe loyendetsa chisankho la MEC likuchitira kalembera wa chisankho.
A Jolobala ati: “NRB siinatsegule centre ina iliyonse ku Machinga kuti anthu azikalembetsapo. Kodi kumeneko ndi kutsatira chigamulo cha khothi? Kodi atsegula liti popeza nthawi yomwe adzitsegula ikhala kuti gawo loyamba la kalembera yatha?”
Gawo loyamba la kalembera wa voti likuyembekezeka kutha pa 3 November chaka chino.
Koma NRB yati itsegula malo olembetsera kaundula wa nzika owonjezera ngati njira imodzi yotsatira chigamulo cha bwalo lalikulu.
Read also: High Court in Blantyre Temporarily Halts Kalibu Academy’s Application Against Kachanga Mosque Azan
Read also: Government launches integrated typhoid vaccine campaign
Read also: Ndindi Mally reignites his voice for the voiceless with a stirring performance at Masintha Ground

