Mwambo wokumbukira malemu Chilima uli pa 10 June.

Timukumbukire Chilima ngati dziko tonse–Kunkuyu

Pa 10 Juni 2024, dziko la Malawi lidali pa chisoni chachikulu chifukwa cha ngozi ya ndege yomwe idachitika mu nkhalango ya Chikangawa mu boma la Mzimba, kum’mawa kwa mzinda wa Mzuzu.

Ndege ya Malawi Defence Force (MDF) ya mtundu wa Dornier 228, yomwe idanyamula yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr. Saulos Klaus Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu (8), idagwa ndipo aliyense mu ndegemo adafera pompo zomwe zinali zoopsa kwambiri m’dziko muno.

Malingana ndi zomwe Our News Platform Mw yapeza, aku banja la malemu Chilima akonza mwambo wokumbukira malemu Chilima ndi anthu ena 8 ku Nsipe m’boma la Dedza kwawo kwa Chilima pa 10 June 2025.

Izitu zichitika ngakhare boma nalo likufuna kuchititsa mwambo ngati omwewu ku Mzimba.

Moses Kunkuyu, mneneri wa boma wati boma likufuna kuti mwambowu ukhale umodzi ndipo uzikhala ndi mbali zonse zokhuzidwa ndi cholinga chobweletsa mtendere m’dziko.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *