Wolemba: Mabvuto Kalawa, Malawi Freedom Network
Wothandizira Episkopi wa Mpingo wa Katolika mu Lilongwe, Bishop Vincent Mwakhwawa, wapempha Akhristu a ku Nathenje Parish kuti azikumbukira kupembedza Ukaristia nthawi zonse.
Bishop Mwakhwawa ananena izi pa mwambo wa mapemphero opembedza Ukaristia womwe unachitikira ku Parish ya Nathenje. Iye anati kupembedza Ukaristia ndi chinthu chofunika kwambiri kwa Akhristu a Katolika, ndipo kumatidalitsa.Diplomatic Passport Scandal in Malawi: Questions Surrounding Nir Gess and Abuse of State Privileges
Pamwambowu, Bishop Mwakhwawa anapemphanso makolo a mpingo kuti azigwira ntchito molimbika kuti atukule mabanja awo, mpingo, komanso dziko. Iye anati n’zomvetsa chisoni kuona Akhristu ambiri ali aulesi.
Analangizanso makolo kuti azitumiza ana awo kusukulu, osati kuwakakamiza kukwatiwa ali aang’ono. Kafukufuku wasonyeza kuti kum’mawa kwa Boma la Lilongwe, ana ambiri amasiira sukulu panjira, zomwe ndi zoopsa kwa mpingo komanso boma.
Polankhula ndi olemba nkhaniyi, Bishop Mwakhwawa anati ndiokondwa kuona mmene Nathenje ikutukira. Atafunsidwa ngati pali maganizo obweretsa ma deacon okhazikika, iye anati diocese ilibe ndondomeko yoteroyo pakadali pano. Komabe, alipo maganizo otsegula masukondale ambiri komanso masukulu aukachenjedwe kuti achepetse umbuli.
Pa mwambowu, Mfumu ya Parish, Fr. Thomas Kasiya, anathokoza Bishop Mwakhwawa chifukwa chopezeka nawo. Iye analonjeza kuti adzakhala pansi ndi komiti yawo kukonza tsiku lapadera lopembedzera Ukaristia monga momwe Bishop walangiziraMassive Soya Bean Theft Uncovered: Police Recover K42.2 Million Worth of Produce, Two Arrested.
Mayi Patricia Ngozo, amene anaimira Akhristu komanso ndi wapampando wa Bungwe la Amayi, anathokozanso Bishop Mwakhwawa chifukwa chopezera pemphero ku parishyi. Iye anati ulendowu walimbikitsa chikhristu cha Akhristu.
Mayi Ngozo analonjeza kuti Akhristu apitiriza kugwirana manja ndi Fr. Thomas Kasiya pa chitukuko ndi kuuzimu. Anatinso apitiriza kulangiza ana kuti asamasiire sukulu panjira, ndipo ali ndi masomphenya oti akhazikitse mabizinesi ang’onoang’ono kwa azimayi kuti akhale odzipatsa okha.
Nathenje ndi imodzi mwa maparish omwe ali mu Archdiocese ya Lilongwe, ndipo ili mu Deanery ya Likuni limodzi ndi Mlaire ndi Likuni. Parishyi ili ndi madera asanu ndi limodzi, omwe ndi Makanya, Chamadenga, Kapedzera, Matapila, Chitekwere, ndi Nathenje.Government Launches Anti-Corruption Strategic Plan to Strengthen Transparency and Accountability in Malawi