Achinyamata Pewani Kugwiritsidwa Ntchito Ndi Anthu Andale –Msusa

Archbishop Thomas Luke Msusa walangiza achinyamata m’dziko muno kuti apewe kugwiritsidwa ntchito ndi anthu andale kuti adzichita ziwawa komanso kubweretsa chisokonezo pamene nthawi ya zisankho yayandikira.

Msusa amayankhula izi Lamulungu ku St Bernadette Kadikira Parishi komwe achinyamata akatolika ochokera m’ma tchalitchi onse omwe ali pansi pa Archdiocese ya Blantyre anasonkhana kuti apemphere limodzi komanso kusinkha-sinkha za maitanidwe mumpingo.

Msusa anati achinyamata akuitanidwa kufesa mbewu za chiyembekezo ndi mtendere pakati pa anthu , komanso akuyenera kukhala amakhalidwe abwino ndi achitsanzo kwa ena potsatira chitsanzo cha bwino cha Yesu Khristu yemwe ndi m’busa wabwino.

Poyankhula ndi Hot Current Affairs atantha mapephero, Ambuye Msusa anati nthawi ya misonkhano yokopa anthu, achinyamata ambiri amakhala pa kalikiliki kudzipenta makaka azipani komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo zomwe zimapangitsa kuti adziyambitsa chisokonezo kapena kuzunza anthu omwe ali osemphana nawo

Related Posts

DPP Blues Rebels Brings Division In

The way Charles Mchacha is castigating the Leader of Opposition in Parliament, Hon Kondwani Nankhumwa, is just testimony enough that Read more

David Bisnowaty Israeli-Born Malawi Parliament Member: Actions, Not Words, Will Change Africa for the Better

Malawi MP David Bisnowaty. How does the Israeli-born son of an eastern European Holocaust survivor end up as a parliament Read more

Mustag Chothia, Sulema Ismael Karim In Land scam

Land remains one area that Malawians know has been heavily abused, characterised by ownership wrangles, not to mention corruption, fueled Read more

David Bisnowaty former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country

Political cum and former Member Of Parliament for Lilongwe City Centre break silence on political situation in the country https://youtu.be/S20UYlVcHs8

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window