Anthu ochita ziwonetsero ati a Chakwera atule pansi udindo

Anthu okhudzidwa omwe akudana ndikukwera kwa mitengo ya zinthu mumzinda wa Blantyre ati apempha mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera kuti atule pansi udindo wawo kamba kolephera kusintha dziko lino monga momwe analonjezera.

Onthuwa anatsogoleredwa ndi Oliver Nakoma.

Anthuwa adayamba kuyenda kuchokera ku Roundabout ku Limbe kudzera ku Masauko Chipembere Highway kupita ku ofesi ya mkulu wa boma ku Blantyre.

Ndipo chitetezo chinali chokhwima chifukwa kunali apolisi ambiri. “`

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *