Chisa Isangalala ndi anthu aku Chikwawa

By: Felix Van Captain Oggess

Anthu okhala mmudzi wa Biyala kwa mfumu yayikulu Ngabu ku Chikwawa apephedwa kuonetsa chikondi komanso kukhala bwino ndi anzawo mu nyengo ino yomwe a khirisitu amakumbukira infa komanso kuuka kwa Ambuye Yesu Khirisitu.

Mkulu wa sukulu ya nkombaphala ya Chisa, a Michael Ndelemani ndi omwe anayakhula izi pomwe sukuluyi mogwirizana ndi anthu ena imasangalala nyengo ya kuuka kwa ambuye Yesu khirisitu mmudzi mwa Biyala mbomali.

Iwo anati ndikofunika kuti anthu alingalire za chikondi chomwe Yesu anationetsera ndipo akhale achikondi kwa anzawo pofunirana mafuno abwino. Powonjezera apo a Ndelemani anati sukulu ya Chisa inachiona cha nzeru kuti pomwe ikupereka maphunziro a nkombaphala kwa ana ang`ono angawanenso mawu opatsa moyo ndi makolo omwe amalera anawa.

Poyakhulapo a Enock Biyala omwe ndi mfumu ya mudziwu anati ndi osangalala ndi zomwe sukulu ya Chisa yapanga ponena kuti izi zapangitsa anthu ochuluka kubwera pamodzi kudzanva mawu a chauta zomwe zipangitse kuti pakhale kudalirana pamene akugwira tchito zosiyasiyana za chitukuko.

Mwazina ku mwambowu kunali ubatizo, kudyera pamodzi, kugawana mawu a Mulungu, Kuvina, masewero a mpira komanso kuonera kanena wa masautso a Yesu Khirisitu.

Kupatula kupereka maphunziro kwa ana a nkombaphala, sukulu ya Chisa imaphunzitsanso amayi maluso osiyanasiyana kuti akhale odzidalira komanso kugwira ntchito ndi achinyamata madera a kumidzi.

Sukulu ya mkombaphala ya ulere ya Chisa inatsekulidwa m`chaka cha 2018 pofuna kuchepetsa mavuto omwe ana okhala madera akumidzi amakumana nawo. Sukuluyi ikupezeka maboma a Chiradzulu, Balaka komanso Chikwawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *