Kaswili Wosewera Ku Wanderers Asaina Mgwilizano Ndi Nyasa Big Bullets

1 min read

Katswili yemwe wachoka kumene kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers Fc Yamikani Chester, akuyembekezereka kusaina m’gwilizano ndi timu ya Nyasa Big Bullets nthawi ina iliyonse.

Malingana ndi mphekesera zomwe wailesi ino yapeza, osewerayu wamvana ndi akuluakulu ena atimu ya Nyasa Big Bullets ndipo aphunzitsi ena atimuyi auzaso akuluakulu kuti asaine osewerayu asanapite ku timu ina.

Chester sanamvane ndi timu yake ya manoma pankhani yokhudza ndalama.

Yamikani Ma Busy Chester akhala akukumana ndi akuluakulu oyendetsa timu ya Nyasa Big Bullets posachedwapa.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours