Moto Wakolera Pomwetsa Zigoli

Mpikisano wa omwetsa zigoli mu ligi ya TNM Super League wayamba kukolera moto mu sabata ya nambala 8 ya mpikisanowu pomwe anyamata atatu omwe ali pa ndandanda wa omwe akumwetsa zigoli zambiri akoleka ziwiri aliyese kumapeto a sabatayi.

Anayambitsa zonsezi ndi Emmanuel Saviel Jr pomwe anamwetsa zigoli ziwiri pa masewero amene timu yake ya Civil Service United imakumana ndi Chitipa United omwe anathera 3-1 mokomera Civo.

Izi zinapangitsa kuti Saviel Jnr afike pa zigoli 6.

Komatu zikuoneka kuti Isaac Msiska wa Mzuzu City Hammers, nkhaniyi sanailandire bwino chifukwa naye loweluka anazitengera mpaka kuchinya zigoli ziwiri timu ya Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Mzuzu.

Zigolizi zapangitsa kumusuntha naye kuti afike pa zigoli zisanu ndi chimodzi kufanana ndi Saviel Jnr.

Nkhaniyi itafika ku waya wa Kamuzu Barracks, Zeliat Nkhoma, anapuputa mfuti yake bwino ndipo waigwiritsa ntchito pomwetsa zigoli ziwiri pa masewero amene amasewera ndi Mighty Tigers.

Pakanali pano, Nkhoma ali ndi zigoli 7 ndipo akutsogolera omwetsa zigoli.

Izi zikutanthauza kuti akatswiri atatuwa ndi omwe ayaka moto pomwetsa zigoli mu TNM Super League.

See also  Biography Of Zuneth Sattar

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *