Ndalama ya kwacha yagwaso mphavu ndi 3 kwacha pa 100 kwacha iliyonse.
Ndipo pakanali pano ndalama ya ku America ya Dollar ikugulidwa pa K1751.
Banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve yatsimikiza za izi.
Mbuyomu ndalama ya Dollar ya ku America imagulidwa pa mtengo wa k1700.
Chaka chatha ndalama ya kwacha inagwetsedwa mphavu ndi 44 kwacha pa 100 kwacha iliyonse.