Bushiri Afikira Mabanja 1200 Ndi Chimanga Ku Mangochi

Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG) Prophet Shepherd Bushiri wapereka chimanga kwa maanja oposera 1200 omwe akuvutika ndi njala m’boma la Mangochi.

A Bushiri ati akudziwa kuti anthu ambiri akufunika thandizo la chimanga m’madera ambiri m’dziko muno ndipo ati ichi nchifukwa chake akupitilira ndi ntchito yogawa chimangachi.

Iwo ati ntchitoyi ifikira maboma onse a dziko lino ndipo apempha anthu ena onse akuchita ntchito ya mtunduwu kuti apitirize pofuna kufikira a Malawi ochuluka omwe akuvutika ndi njala.

“Galimoto za mtundu wa truck zopitirira khumi zili kale m’maboma a Dowa, Rumphi, Nkhotakota ndi ena komwenso tikhale tikufikira anthu ndi thandizo la chimanga, choncho ndipemphe anzanga ena omwe akupanga ntchito yofanana ndi yomwe tikugwira kuti tigwirane manja pofuna kuombola Malawi,” atero a Bushiri.

Mmodzi mwa anthu omwe alandira nawo thandizoli a Dorcas Baluti a mdera la mfumu yaikulu Namkumba ayamikira a Bushiri kamba kathandizoli ponena kuti liwapulumutsa ku njala yomwe ikuwasautsa kamba koti chimanga chomwe adalima m’minda yawo chidauma kamba ka ng’amba yomwe inali m’dziko muno.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *