Ntchito yosaka ndege yayima mpaka mawa

Pakadali pano, Ntchito yosaka ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino yayamba yayima kaye kufikira mawa mamawa nthawi ya 6 koloko.

Izi zili chomwechi kamba kakusowekera kwa zipangizo zochitira kafukufuku.

Zadziwikanso kuti anthu omwe akuchita kafukufukuyi akugwiritsa ntchito uthenga omwe anthu akumadera komwe kukuganizilidwa Kuti kwagwera ndegeyo akumawapasa.

Makono, maiko otukuka amagwiritsa ntchito tindege takafukufuku (Searching Drone ) ena matitchura kuti Rescue Drones.

Ma drone Ngati awa ali ndi lenzi yayikulu yomwe amatha kuwona patali akamauluka komanso ali ndikuthekera kuwunikanso ngakhale mmadzi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *