Panabvuta Ndi Pati Kuti Ndege Yonyamula Wa Chiwiri Kwa Mtsogoleri Itsatsatiridwe?–Kaliati

Kaliati yemwe akuyankhula kwa atolankhani wati chipani pachokha chikusaka komwe kungapese ndegeyi.

Koma Kaliati watsindika kuti chipani chili ndichiyembekezo kuti mtsogoleri wachipani-chi abwerera bwino.

Kaliati wapempha wotsatira chipani cha UTM komanso a Malawi onse kuti adekhe.

Mwazina, Kaliati wati zikupereka mafunso kuti pakuvuta ndipati kuti ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wachipani cha UTM isatsatiridwe.

Patricia Kaliati wati chipanichi chikuphemphera komanso kukhulupilira koti mtsogoleri wachipanchi ndi otetezeka.

Kaliati wapempha anthu akufuna kwabwino komanso mayiko kuti athandize ntchito yofufuza ndegeyi.

Iwo apempha otsatira chipanichi kuti adekhe ndikusatira bwino pa ntchito yofufuza ndegeyi.

Yemwe anali mtsogoleri wachipani cha UDF Atupele Muluzi nayenso wafika ku office za UTM komwe kuli msonkhano wa olembankhani.

Muluzi alinso limodzi ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UDF mchigawo chapakati, Michael Antonie.

Mlembi wamkulu wachipani cha UTM, Patricia Kaliati, wati chipani chawo ndichokhumudwa ndikusowa kwa ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Saulosi Chilima.

Ngakhale kuti wayamikira kuchirimika kwaboma komanso ena pofuna kupeza komwe ndege- yi ili, Kaliati wati chipani cha UTM ndichokhumudwa ndikuchedwa kuyamba kusaka ndege.

Iye wati chipani chikuyembekeza kuti adindo oyenera apereka uthenga wokwanira kwa aMalawi.

Malinga ndi Kaliati boma silinawauze chilichonse chipani chawo zankhani-yi.

Chipani cha UTM chati chikufufuza m’madera ena monga Dwambazi, Kasungu komanso Mchinji ndipo akuti chipanichi chapeza ndege yamtundu wa Helicopter kuti ithandize kafukufukuyu.

M’mawu ake Felix Njawala, ofalitsa nkhani za chipani cha UTM wati kafukufuku yemwe akuchitika akupelewera.

A Njawala ati chipani cha UTM chapeza kanema yemwe akuonetsa ndege zonse zomwe zinayenda lolemba kupatulapo yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima.

Iwo ati atumiza magulu anayi omwe ena apita ku Nyika komanso malo ena kuti afufuze komwe ndegeyi Ili, kupatula kulunjika mu nkhalango ya Viphya yomwe imadziwika kuti Chikangawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *