Olowa Kumene Adikire Zaka Ziwiri–MCP

MUNTHU AMENE WANGOLOWA KUMENE MU CHIPANI CHA MCP ALIBE MWAYI OZAPIKISANA PA ZISANKHO MU KOMITI YAIKULU CHAKA CHINO

Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chamanga mfundo yoti yemwe akufuna mpando mu komiti yaikulu ya chipanichi adzikhala kuti anakhalapo pa udindo mchipanichi kwa zaka ziwiri.

Anthu ena omwe atitsina khutu, ati komiti yaikulu ya chipanichi ndi yomwe yagwirizana izi pa msokhano wake omwe inachititsa lero mu mnzinda wa Lilongwe.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, yemwenso ndi pulezidenti wa chipanichi, anali nawo pa zokambilanazo.

Otitsina khutuwo, omwe anali nawo pa nkumanowo koma anapempha kuti tisawatchule, ati mmodzi mwa nthumwi anabweretsa mfundoyi kugulu ndipo ena anaiikila kumbuyo, kenako komitiyo nkuivomereza.

Iwo anati zaka ziwirizo zikhale zoti munthu anakhalapo pa mpando uli onse omwe unakhazikitsidwa mu malamulo aakulu a chipanichi.

Izi zikutanthauza kuti anthu ongolowa kumene mchipanichi alibe mwayi opikisana nawo pa zisankho za komiti yaikulu zomwe zichitike chaka chino.

Pakali pano mneneri wa MCP a Ezekiel Ching’oma akana kuikapo mlomo pa nkhaniyi.

Iwo ati chipanichi chitulutsa kalata yofotokoza tsatanetsatane wa zomwe akambiranazo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *