
MCP General Membership Idabwa Ndi Ulamuliro Wa Chakwera
Mchithunzi, Kantukule kulandira President Chakwera pa Kamuzu International Airport}.
Gulu lomwe likudzitchula kuti General Membership of Malawi Congress Party laonetsa kudabwa kuti President Lazarus Chakwera adasankha nduna yaza ntchito Vera Kantukule kuyang’anira dziko pomwe ankapita ku Mozambique m’mwezi wa April chaka chino chikhalirecho ndunayi siya MCP komanso ilibe udindo ulionse mchipanichi.
Iwo akuti a Chakwera akanatha kusankha amai ena mchipanichi omwenso ali nkuthekera pomwe ati pa ndale mtsogoleriyu adaphonya.
Izi ndi malinga ndi kalata yomwe gululi latulutsa pomwe latinso anthu ochulula omwe analembedwa ntchito ku nyumba ya boma {State House} ndi a mpingo wa Assemblies of God.
Kalatayi yomwe yasainidwa ndi m’neneri wake, Zinenani Magola komanso wapampando, Alex M...