Zathera ma hiii ndi ma haaa ku Mzuzu

Timu ya Moyale Barracks yalepherana ndi Timu ya FCB Nyasa Big Bullets mumasewero amu ligi ya TNM Super League pa masewero omwe analipo masanawa pa bwalo la Mzuzu.

Matimu onse amaonetsa njala yofuna kumwetsa chigoli koma kungoti thupi silimamvana ndi mtima zomwe umafuna chifukwa nde kunali kuphonya mwam’nanu.

Oyimbira masewero opatsidwa chilolezo ndi FIFA, Newton Nyirenda, atawona kuti mphindi 90 komaso 4 zowonjezera zatha analiza wenzulo kutsimikiza kuti zoonadi mamuna nzako mpachulu mkulinga utakwerapo.

Pamasewerowa, otchinga kumbuyo ku Moyale Barracks, Maneno Nyoni, ndiyemwe anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa osewera onse.

Pakanali pano, timu ya FCB Nyasa Big Bullets ili ndi ma points 14 pamasewero 8 omwe yasewera pamene Moyale Barracks ili pa nambala 6 ndi mapoints 11 atasewera masewero 8.

Lamulungu lomwe likudzali pa bwalo la Kamuzu mu nzinda wa Blantyre kuli mkoke-mkoke pomwe FCB Nyasa Big Bullets ikhale ikukumana ndi Silver Strikers ndipo pa uwiri wawo sanagonjepo chiyambileni 2024 TNM Super League.

Pamene Moyale Barracks ikhale ikukumana ndi Mighty Tigers ba bwalo la Mzuzu loweluka likudzali.

Related Posts

Malawi Freedom Network advice President Banda to fight corruption

If you thought Malawians are lazy people, I bet you a Dinosaur, think twice and you will know, check in Read more

David Bisnowaty Israeli-Born Malawi Parliament Member: Actions, Not Words, Will Change Africa for the Better

Malawi MP David Bisnowaty. How does the Israeli-born son of an eastern European Holocaust survivor end up as a parliament Read more

Biography Of Zuneth Sattar

Zuneth Sattar Director of Xaviar Limited and Xaviar Investments Limited Zuneth Sattar is an experienced and knowledgeable property investor. With Read more

Zuneth Sattar Is An Experienced Property Investor

PROPERTY INVESTOR PROPERTY MARKET AN OVERVIEW This blog will cover a wide range of topics and subjects that relate to Sattar’s Read more

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window