Anthu m’dziko muno awatsimikizira kuti utsogoleri wa Tonse ukuchita chilichonse chotheka kuti uthane ndi mavuto aza chuma ndi chisamaliro omwe akuta dziko ndipo kuti akhale ndi chiyembekezo.
Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera wabwerezanso kutsimikidlzira a Malawi Lachiwiri ku Mzuzu pomwe amafika mchigawo chakumpoto komwe ayendere mbewu m’minda, kuchititsa misonkhano yachitukuko m’maboma ena ndi kulonga ufumu a Joseph Bongololo Gondwe kukhala Paramount Chief Chikulamayembe ku Rumphi.
Iye anafotokoza kuti akudziwa mavuto omwe anthu akukumana nawo koma waŵatsimikizira kuti akhale ndi chiyembekedzo poti mavutowa atha ndipo dzikoli lidzakhala lodzidalira pa lokha.
Chakwera, yemwe anafika pa ndege ku Mzuzu, anati cholinga cha maulendo ake ndi kulondoloza ntchito za chitukuko zomwe boma likugwira chifukwa mayankho a mavuto ena omwe dziko lino likudutsamo ndi ofunika kupanga katundu, ulimi komanso kukhala ndi misika yokhadzikika.
Ngakhale zili choncho, akatswiri ena ati maulendowa akutha ndalama chifukwa nduna za boma zitha kugwira ntchito zinazi.