Wednesday, February 28
Shadow

Chipani Cha DPP Agwirizana Kuti Nankhumwa akhalebe pampandowu.

Kusamvana komwe kunalipo m’chipani cha DPP pa yemwe akuyenera kukhala mkulu wa zipani zotsuta boma m’nyumba ya malamulo kwatha tsopano.

Izi zikutsatira m’gwirizano omwe mbali zokhuzidwa zapanga kuti a Kondwani Nankhumwa akhalebe pampandowu.

Malingana ndi mneneri wa chipani cha DPP, Shadrec Namalomba, a Nankhumwa akhalabe pa udindowu kufikira pomwe chipanichi chidzachititsenso chisankho china cha mtsogoleri wa zipani zotsutsa m’nyumbayi.

“Tinafunsa bwalo la milandu kuti litipatse nthawi yomwe tingakhale titachitanso chisankhochi, koma wodandawula anakana kuti izi zisakhudzee bwalo la milandu,” yatero kalata yomwe a Namalomba atulutsa.

Ganizoli ladza kutsatira zokambirana zomwe zachitika ndipo mkhala pakati wake anali oweluza milandu, Kenyatta Nyirenda.

Kusamvanaku kunadza, pomwe aphungu ena a DPP anasankha a George Chaponda kukhala pa udindowu pa mkumano wawo wina ku nyumba ya mtsogoleri wa chipanichi, Peter Mutharika ku Mangochi.

Aphungu ena sadakondwe ndi izi ndipo anakamang’ala ku bwalo la milandu.

Mbali ya a Chaponda akuti yavomerezanso kuti inalakwitsa kuwasankha pa mpandowu popanda aphungu ena.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *