Sitikupanga Nawo Ena Alandira K60 Million

FB IMG 1666940550032

Gulu lina lomwe likudzitcha kuti Civil Society for Unity of Purpose ladzambatuka ku Lilongwe komwe likuti silitenga nawo gawo pazionetsero za mawa ponena kuti omwe akonza zionetserozi alandira ndalama ku zipani zotsuta.

M’neneri wa gululi, Agape Khombe, yemwe m’mbuyomu adali ku gulu la Mbadwa Zokhudzidwa, akuti omwe akutsogolera zionetserozi alandira K60 million.

Koma Khombe analephera kupereka umboni kwa olemba nkhani pa nkhani-yi ngakhale anati anthu ena masiku ano akugwiritsa ntchito zionetserozi pofuna kupeza zofuna zawo.

Koma omwe akonza zionetserozi zadayankhepo pa izi.

Mwa zina, zionetsero za mawa ku Lilongwe zikufuna kukapereka madando kwa President Lazarus Chakwera ku nyumba ya chifumu pa mavuto omwe akuta dziko lino kuphatikizapo katangale.

Gulu la Action Against Impunity ndi lomwe likutsogolera zionetserozi.

0 0 votes
Article Rating
Subscribe
Notify of
guest
0 Comments
Oldest
Newest Most Voted
Inline Feedbacks
View all comments
0
Would love your thoughts, please comment.x
()
x