Jimmy Joseph Kalekeni Nkasa anabadwa pa 3 DisembaIa mu 1967 m’boma la Zomba. Iye anabadwira m’dera lotchedwa Moleni ndipo ndi wachitatu kubadwa m’banja la ana anayi (amuna awiri ndi akazi awiri).
Katswiriyu anabadwira m’banja losauka zedi ndipo ali wachichepere amagwira maganyu n’cholinga choti azipeza zinthu zina m’moyo. Bambo ake anali woluka malichero ndi mabasiketi. Bambowa anaphunzitsa mwana waoyu lusoli ndipo anali kuthandizana kuti banja lizipeza chakudya.
M’zaka za m’ma 1970, makoIo ake anapeza maIo m’boma Ia Machinga. Banjali linakhazikika kwa mfumu yaikulu Sitola. Izi zinachititsa kuti boma la Machinga lisandukenso kwao.
Chifukwa chosowa chithandizo cha chuma, Joseph sanapite patali ndi sukulu. Iye anaisiya ali sitandade 8.
Nkasa anayamba kuyimba ali wachichepere mu ‘choir’ ya mpingo omwe ankapemphera otchedwa Full Gospel Church of God. M’chaka cha 1999 kunali msonkhano wapachaka wampingowu ndipo ‘choir’ yake linayimba modabwitsa kuposa ena. Izi zinachititsa kuti Nkasa apeze mwayi ndikuthandizidwa. Anthu omwe anali pamwamboyu anasonkha ndalama ndi zovala n’kumupatsa. Kenako, anajambula chimbale chake choyamba chauzimu pogwiritsa ntchito ndaIama yomwe anthu achifundowo anamupatsa.
Asanatulutse chimbale cha Wayenda Wapenga, Phungu anali atatulutsa kale zimbale pafupifupi zisanu. Zina mwa izo ndi Ndigwireni Dzanja, Kutha Kwafika, Messiah ndi Kupupuluma. Kuchokera pa chimbale cha Wayenda Wapenga, Nkasa watulutsa zimbale zina zoposa zinayi ndipo zina ndi monga Mizimu, Mamillionaire ndi Tigwirane Manja.
Katswiriyu amatchuka ndi dzina loti phungu chifukwa cha malangizo omwe amapezeka m’nyimbo zake.
Nkasa ali pabanja ndipo anadaIitsidwa ndi anayi asanu ndi atatu.